Kulapa: Khomo la Chifundo

Wokondedwa Moyo'we: Kodi ukudziwa kuti wapezeka wochimwa ndi Mulungu Woyerayo, ndi kuti kwaikidwa kwa iwe kufa? Ngati munthu wochimwa afuna kuithawa imfa ya muyayayi ndi kupulumutsidwa ku nthawi zosatha, iye ayenera kulandira chifundo cha Mulungu'chi. Chifundo chimatiteteza ife pa chirmene tikadalandira. Komatu Mulungu samangoika chifundo chake pa anthu popanda choyenereza ayi, ngakhale kuti chipulumutso nchaulere, chopanda mtengo wake (chosagula) ndiponso chosati nkuchigwirira ntchito. Chotiyenereza chakuti Mulungu atipatse ife chifundo chake chipezeka mu liu limodzi lokha: Lapani.

Yohane Mbatizi anadza nalalikira Mau a Mulungu ndipo uthenga wake unali wokhweka, koma wamphamvu. "Lapani inu chifukwa ufumu wakumwamba wayandikira" (Mateyu 3:2). Yesu, Mwana wa Mulungu, anayamba utumiki wake ndi uthenga womwewo, "Lapani pakuti ufumu wakumwamba wayandikira" (Mateyu 4:17). Kulapa ndicho chotiyenereza cha chipulumutso monga Mtumwi petro ananena, "Chifukwa chake lapani, bwererani kuti afafanizidwe machimoanu" (Machitidwe 3:19). Kulapa ndi khomo loyenera kutsegulidwa ngati chifundo chingaonjezedwe ndi chipulumutso kupatsidwa.

Mdziko lapansi lathuli muli unyinji wa anthu, bwenzi langawe, mnjira zambiri timasiyana wina ndi mnzake. Komabe pali mbali ina imene tonse pamodzi timagawana popanda wotsala. Mau a Mulungu amationetsera ife bwino mbali imeneyi pamene amati: "Pakuti ONSE anachimwa naperewera pa ulemerero wa Mulungu" (Aroma 3:23). Ndipo tamveraninso, "Palibe M'MODZI wolungama, inde palibe m'modzi" (Aroma 3:10). Mulungu ananena kupyolera mwa mneneri wake Yesaya ndi kuti, "Tonse tasochera ngati nkhosa, tonse tayenda yense mnjira ya mwini yekha" (Yesaya 53:6). Kodi ulikudziwa cholinga chenicheni cha malemba oyerawa? "ONSE anataika". "PALIBE wolungama". "ONSE anachimwa". Wokondedwa wowerenganu, kodi ichi sichili kukukhudzani? Mzimu wanu, mayo wanu ndi za Mulungu. Mwamuna kapena mkazi ngakhale mwana kapena wamkulu amene sazindikira Mulungu monga mwini wa moyo wake aneneyo ali mkusamvera ndi mtchimo. "Moyo wochimwawo ndiwo udzafa" (Ezekieli 18:4).

Machimo anu akulekanitsani inu ndi Mulungu. Mumamva kufunafuna mkati mwanu kotero kuti simungathe kukufotokoza ayi. Mungathe kuona ngati ndinu wotayika ndi kuti Mulungu sakumva. Chifukwa chake Mulungu achitchula, "Taonani mkono wa Yehova sufupika, kuti sungathe kupulumutsa; khutu lake silili logontha, kuti silingamve; koma zoipa zanu zakulekanitsani inu ndi Mulungu wanu; ndipo machimo anu abisa nkhope yake kwa inu kuti lye sakumva" (Yesaya 59:1-2). Ndiponso, "Mphotho yake ya uchimo ndi imfa" (Aroma 6:23). Pamene muli kulingilira za moyo wanu ndi machimo anu, lingiliraninso za Mulungu. Mulungu alibe tchimo, choncho lye ndi Woyera, wolungama ndi wolunjika. Mulungu amati tchimo liyenera kuweruzidwa. "Pakuti Mulungu adzaweruza mlandu wa zochita zonse, ndi zobisika zonse, kaya zabwino ngakhale zoipa" (Mlaliki 12:14). Pali phompho lalikulu loikika pakati pa inu ndi Mulungu, ndi imfa yamuyaya, pokhapokha titapeza njira yomwe ipyola phompholo ndi kukoka wochimwayo pa maso pa Mulungu Woyerayo (Luka 16:26). lnde ilipo njira, chilipo chiyembekezo chanu!

Nkhani yonse ya: Kulapa: Khomo la Chifundo

Pamene tiona kuti Mulungu anaika chiweruzo cha imfa chifukwa cha tchimo, lyenso ndi Mulungu wachikondi. "Mulungu ndiye chikondi" (1 Yohane 4:16). Mulungu akukondani, mnzanga, ngakhale mukukhala mu uchimo. Chikondi chake chidakukonzerani njira yoti mupulumutsidwe nayo (Yohane 3:16). Mulungu, wosanamayo, adzaika chiweruzo chake pa tchimo, ndipo ngati chilungamo chake sichidzakhala pa munthu, pomwepo iye adzafa. Chomwecho Mulungu safuna wina aliyense kuti ataike, anatuma Mwana wake Yesu kutitengera thonzo la uchimo kuti tikhale ndi moyo. Malemba akuti, "Chifukwa chake onani chifatso chake ndi kuuma mtima kwake kwa Mulungu" (Aroma 11:22). Ubwino wa Mulungu ndi wakuti apulumutse munthu koma chiweruzo chake chinkafuna chilango.

Yesu anadza ku dziko lapansi ndi cholinga chakuombola miyoyo yathu. Iye ndi Woyera ndi wopanda tchimo, Mwana-wa-Nkhosa wa Mulungu wopanda chilema. Chikondi cha Mulungu chapa ife chinaoanekera pamene lye anatenga machimo athu ndi kulakwa kwathu ndi mphotho yake ya imfa ndi kuziika izi pa Yesu. Taonani ubwino wake! Ndipo monga Yesu anamvera chifuniro cha Atate wake, lye analandira mphotho ya machimo athu. Yesu anakhala wochimwa m'malo mwathu ndi kukwaniritsa chiweruzo cha Mulungu. Iye anapachikidwa pa mtanda pa maora asanu ndi limodzi (6 hours) namva kuwawa ndi ululu kufikira mphotho yake ya machimo athu itaperekedwa, ndipo pamenepo Yesu anafa. Taonani kuuma mtima kwake kwa Mulungu!

Wokondedwa wowerenganu, kodi mukuona kuti Yesu anakuferani inu, ndi kuti lye anafa CHIFUKWA cha machimo anu? Kodi makamaka yemwe adapachika Yesu ndani? Kodi amene anakhudzidwa ndi akuluakulu a Ayuda, kapena Pilato kapena asilikari a Aroma okha? Petro mtumwi tsiku lina analalikira kwa chikhamu cha anthu zikwizikwi. Uthenga wake wa Petro unali woona: "lye (Yesu), anaperekedwa ndi chikhamu komanso ndi nzeru ya kudziwiratu ya Mulungi, INU munamtenga ndi manja anu oipawo munampachika ndi kumupha" (Machitidwe 2:23). Wokondedwa moyowe, yang'anani kwa Yesu yemwe anapachikidwa ndipo bvomerezani kulakwa kwanu ndi kuchita naye mu imfa yake!

Kulapa koonadi kumayambira makamaka pa mfundo imeneyi, pamene musunga mu mtima mwanu za malo owopsyawo ndi zomwe zinachitikazo. Ndi mphamvu ya Mzimu wa Mulungu mudzazindikira kuti mukanayenera kufa munali inu osati Yesu ayi. Koma Yesu anatenga malo anu! Ngati inu muzindikira ichi mumtima mwanu, kudzakubweretserani chisoni ndi kuti tchimo simudzalifunanso ayi. Pakulingirira kuti wina adakonzera wina imfa ndi chinthudi chochititsa mantha, makamaka kuti lye anali Mwana weniweni wa Mulungu. Miyoyo yomwe imagwira masomphenya awa imalapa ndi kubvomereza machimo awo. Ndi monga momwe tilingirira za chiweruzo cha Mulungu chokhuthulidwa pa Yesu ndipo pakuchidziwa ichi tidayenera kulira ndi ife omwe tidayenera imfa, "Mulungu mundichitire chifundo ine wochimwa" (Luka 18:13). lzi ndi ntchito zoyamba za kulapa. Ngati kulapaku kupitirira, kumakwaniritsa pa kusiyiratu njira zathu zoyamba za uchimozo, ndi kutembenukira ku njira za Mulungu. Munthu yemwe watsukidwa ndi kuyeretsedwa kuchokera ku njira zake zoipazo, iye adzazifulatira izo ndi kutembenukira ku zinthu zakumwamba. ichi mwachidule ndi njira yolapa yomwe imachitika ndi Mulungu mu mitima ya onse akudza kwa lye. Pokhapokha munthu atalapadi, ndiye kuti iye adzadziwa mtendere, chimwemwe ndi kusungika. pokhapokha titachita naye Yesu mu chisoni chake ndi zowawa zake za mu Getsemane pomwepo tidzamva chimwemwe cha kuuka kwake.

Potsiriza penipeni, zotsatira zake za kulapa ndi kukhala woyamika kotheratu ndi kudzipereka kwa Khristu ndi ku chifuniro cha Mulungu. Pa ichi chiphatikizanso Mpingo monga kunaikidwa mu Chipangano Chatsopano. Pamene tinaikidwa kufa ndipo popanda njira yotulukiramo, Yesu anati: "ldzani kwa lne ndipo ndidzakupumulitsani inu" (Mateyu 11:28). "Timkonda ife chifukwa anayamba lye kutikonda" (1 Yohane 4:19).

Lumikizanani nafe.

Pezani mauthenga olembedwa.

Mtendere Wa Mumtima M'dziko La Mabvuto

"Mtendere, uli kuti mtendere - wa maiko athu,  m'nyumba zathu, makamaka mtendere wa mitima yathu?  Kulira kowawitsa moyo uku kulilira mtendere ktwakhala kuli kumvekabe pakati pa mibadwo yonse; komatu kuliraku nthawi zones kukukulira kulira chifukwa cha kuchuluka zochitika padziko zimene zikupangitsa kuti mtendere usowekedi. M'bale ukuwerengawe,  kulira kwa mtima wako ndi kumenekunso kodi? Mkati mwa zosowetsa mtendere ndi zosakhutitsa mtima zonse, kodi umalakalakadi utapeza mtendere wamumtima umene uli opambana zonse?

Zimene zidaoneka monga zinthu zokondweretsa, m'mene akatswiri anayamba kupanga zinthu zaliwiro koposa, katumizidwe ka mau mosabvuta, zochitika zambiri ndi kusintha kwa masiku ano zachititsa dziko ndi anthu kukhala osokonekera. Zinthu zambiri zimene akatswiri anzeru akufufuza-fufuza kuti mwina zingathandize kupanga dziko lapansi kukhala malo abwino kukhalapo zapangitsa moyo kukhala obvuta ndi osokonekera. lnde ngakhale kuti zambiri kwa ife m'moyo uno ndi zosabvuta chifukwa cha izi, zinthu zomwezo zikutipangitsa ife kukhala osowa mtendere ndi osakhazikika m'maganizo ndi m'mitima. Ndife otopetsedwa, ndi odandaula. Ndipo mosabisila. ife tikusowa uphungu ndi chitsogozo, tisowa chitetezo ndi chitsimikizo. Tikusowa, ndipo tikufuna mtendere wamumtima.

Mtendere wamumtima ndi chuma choposa chimene munthu angakhale nacho. Tikaleka kukhala moyo okhumudwa ndi odandaula, ndikuyamba kukhala moyo osadandaula, odekhetsa mtima, ndiye kuti tapeza ngale imodzi mwa ngale zopambana zamtendere. Mtendere wa mumtima umabweretsa chikwaniritso ndi chimwemwe, ndipo ndi gwelo la chilimbitso kwa ife eni ndi anzathu.

Kodi chuma chimenechi chingapezekedi m'dziko lodzala ndi zopinga, zokhumudwitsa, zosokoneza ndi mabvuto ochuluka?

Nkhani yonse ya: Mtendere Wa Mumtima M'dziko La Mabvuto

Kufufuza kweni-kweni kuja kwayamba tsopano! Anthu ochuluka akufuna-funa mtendere wa mtima wao podzipangitsa kukhala otchuka, podzikondweretsa podzipezera mphamvu ndi ulamuliro, popeza maphunziro apamwamba ngakhale mu ukwati momwe. Mitu yao yadzala ndi nzeru, matumba awo adzala ndi chuma, koma mizimu yao ndi yosowa ndithu. Ena akuyesa-yesa kuthawa zoonadi za moyo uno poledzera ndi kugwiritsa ntchito mankhwala ozunguza bongo kuti kapena apeza mtendere, koma samaupeza. Zofuna zao zingowatengera bvuto ndi nsautso; palibe chimene apindula kuti apeze mtendere-akhalabe m'dziko la mabvuto ndi moyo obvutika. Kiyi weniweni pakufunafuna mtendere tikhoza kuupeza m'zigawo izi:

"Titha kukhala nao mtendere koma osalingalira za mkati mwake." Timafufuza m'zinthu za dera zimene tingathe kizigwira ndi kuziona ndi maso, koma timayiwala kuona zamkati. Timakhala ndi mantha pa zoona zimene tingazitulukire. Timafuna kuyika kulakwa konse ndi kusauka kwa moyo wathu pa zo bvuta za dziko lino, kuiwala kuti mumtima mwathu ndi m'mene tingapeze yankho la bvuto lathu. Ndi mumtimamo m'mene machiritso a zobvuta zathu ayenera kuyambira.

Mulungu anapanga munthu ndi Mzimu umene umasowa kukhala mu chiyanjano ndi Mulengi wake. "Monga nswala ipuma wefμwefu kukhumba mitsinje; motero moyo wanga upuma wefuwefu kukhumba lnu, Mulungu. Moyo wanga uli ndi ludzu la kwa Mulungu, la kwa Mulungu wamoyo: Ndikadze liti kuoneka pamaso pa Mulungu?" Sal. 42:1-2. Ndi Mulungu wamoyo yekha, Khristu wamoyo yekha, ndi Mau a moyo okha amene angakhutiritse Mzimu. Ichi chitsimikizike kwa inu kuti ~ simungapeze mtendere padziko ngati inu eni simuli pamtendere ndi Mulungu.

Ngakhale mizimu yathu imalakalaka kuyanjana ndi Mulungu, umunthu wathu wochimwa umapandukira njira yake. Gawo lina la umoyo wathu limafuna Mulungu pomwe gawo lina limatumikira zofuna za kuthupi .. Mitima yathu ili monga chigwa chomenyaniranapo nkhondo yosatha.

Kulimbana kwa mkati uku kumatipanga ife kukhala anthu opanda thandizo. "Koma oipa ali ofanana ndi nyanja yowinduka; pakuti siingapume, ndi madzi ake autsa matope ndi ubve" Yes. 57:20. Sitingakhale ndi mtendere kufikira moyo wathu, maganizo, thupi ndi mzimu zitalumikizana ndi amene anatipanga ndipo amatimvetsetsa ifeyo. Sikuti ndi Mbuye wa dziko lokhayi, koma amadziwa moyo wanu ndi wanga kuyambira chiyambi kufikira mapeto. Ankaganizira za ife pamene anadza padziko lapansi "Kuwalitsira iwo okhala mumdima ndi mthunzi wa imJa; Kulunjikitsa mapazi athu munjira ya mtendere" Luka 1:29. lye monga Karonga wa mtendere, aitana tonse kuti tidze kwa lye. "ldzani kuno kwa lne nonsenu akulema ndi akuthodwa, ndipo lne ndidzakupumulitsani inu" Mat. 11:28. Tikadza kwa lye, tidzapeputsidwa kuzolemetsa zathu ndi kupeza mpumulo mu mtendere umene lye amapereka. Mtendere wathu udzakhala monga mtsinje (Yes. 48:18) umene uyenda nthawi zonse, mtendere umene upambana chidziwits_o chonse Afilipi 4:7. Kodi mubvomera kubwera kwa lye, "Kutula zolemetsa zanu pa lye" kuti mumve lye akuti "Mtendere ndikusiyirani inu, mtendere wanga ndikupatsani; lne sindikupatsani inu monga dziko lapansi lipatsa. Mtima wanu usabvutike kapena usachite mantha." Yoh. 14.27.

Mulungu adalenga munthu ndi kumuika m'munda okongola kuti iye akhale ndi mtendere, chisangalalo ndi chimwemwe. Koma pamene Adamu ndi Eva sanamvere, nthawi yomweyo anatsutsidwa ndi tchimo. Asadachimwe nthawi yonse anafunitsitsa kukhala  ndi Mulungu, koma atachimwa anadzibisa okha mwanianyazi. Kutsutsika ndi mantha zinalanda mtendere ndi chimwemwe zomwe iwo anali nazo poyamba paja. Ichi ndiye chinali chiyambi cha dziko la mabvuto - ndi moyo wa mabvuto.

Bukhu lopatulika litiuza kuti tchimo lakusamverali liri pa ife. "Tonse tasochera ngati nkhosa; tonse tayenda yense m'njira ya mwini yekha; ndipo Yehova anaika pa lye mphulupulu ya ife tonse." Yes. 53:6. "Pakuti onse anachimwa naperewera pa ulemerero wa Mulungu;" Aroma 3:23. Kutsutsika, mantha, kubvunduka, kusalolela, kudzikonda ndi zokakamiza zina za upandu ndi zokuta moyo wathu konse tingapite. Zimabweretsa kutopa ndi kufooka kwa maganizo. Tiyenera kuthokoza kuti Yesu sanadze padziko " ..kuti akaweruze dziko lapansi, koma kuti dziko lapansi likapulumutsidwe ndi lye." Yoh. 3:17. "Pakuti Mulungu anakonda dziko lapansi kotero, kuti anapatsa Mwana wake wobadwa yekha, kuti yense wakukhulupirira lye asatayike, koma akhale nawo moyo wosatha." Yoh. 3:16. "Zinthu izi ndalakhula ndi inu kuti mwa Ine mukakhale nao mtendere. M'dziko lapansi mudzakhala nacho chibvuto, koma limbikani mtima; ndalilaka dziko lapansi lne." Yoh. 16:33.

Undekha (kudzikonda) ndiye chinali chiyambi cha kusamvera. Mpaka lero lino upitilirabe kukhala chida chimodzi cha uchimo chimene chititengerabe ife ku njira yokhumudwitsa ndi yowawitsa mtima. Tikhala odzikonda mu zolinga zathu, timakhala osinkha-sinkha, okhumudwa ndi odandaula. Tikapitilira kuyenda m'njira yodzikondayi, tidzakhala obvutika koposa. M'malo modziyang'ana tokha monga eni ake a moyo, tiyenera kutembenukira kwa Mulungu ndikumulola lye kukhala mwini weniweni wa moyo wathu. Ngati sitilola Mulungu kukhala mwini weniweni wa moyo wathu, ndi kwa pafupi ife kudandaula ndi zinthu zazing'onozing'ono, kudzipangitsa manyazi, kuopa ndi kukhala okhumudwa. Mulungu akakhala pakati pa moyo wathu monga mwini weniweni, moyo wathu wonse udzakhudzidwa monga zikhalira habu ndi masipoko pa tayala la njinga, ndipo moyo wathu udzakhala moyo oyenera ndi okoma. Ndi mtima okhawo okhazikika pa Mulungu umene ukhala wa ngwiro ndi wa mtendere. Olemba Salimo akuti, "Moyo wanga wakhazikika, Inde Mulungu, moyo wanga wakhazikika, ndidzaimba ndi kulemekeza." Ndi chikhulupiriro chonse pa Mulungu, anatha kukondwera ndi moyo wokhazikika. Mitima yathu ikakhazikika pa Mulungu tiri nawo mtendere wa mkati ngakhale tiri pakati pa mabvuto akunja kuno.

Nkotheka inde kukhala "—osautsika monsemo, koma osapsyinjika; osinkha sinkha koma osakhala kakasi;" 2 Akor. 4:8. Mmene Yesu anati, " … kwa ophunzira ake, Ngati munthu afuna kudza pambuyo panga, adzikane yekha, natenge mtanda wake, nanditsate lne." Mat. 16:24, anaitana aliyense kukusinthika kwa moyo wa munthu kumene kuli ndi tanthauzo lalikuru. "Chifukwa chache ngati munthu ali mwa Khristu, ali wolengedwa watsopano, zinthu zakale zapita, taonani zakhala za tsopano." 2 Akor. 5:17. Kodi mubvomera kuyitana kwakeku m'mene ati "ldzani kwa Ine?" lye apatsa kuwala m'malo mwa mdima, chikhulupiriro m'malo mwa chikayiko, mtendere m'malo mwa kubvutika, chimwemwe· m'malo mwa chisoni, mpumulo m'malo mwa kutopa, chiyembekezo m'malo mwa kukhumudwa, ndi moyo m'malo mwa imfa.

Monga makolo athu oyamba aja, tikangolekana ndi Mulungu, mantha ndi kubvutika mumtima zimatikulira mwamsanga. Tikakhazikitsa moyo wathu pa zinthu zosadalilika zadziko lapansi zimene zidzabvunda, chitetezo ndi chikhulupiriro chathu ndi zogwedezeka. Mtendere wathu umasokonezeka.

Chikhulupiriro ndi chiyembekezo ndiye mankhwala eni eni othetsera mantha ndi kubvutika kwa mumtima. Kokoma ndi kopumulitsa ndithu kukhulupirira Mulungu wa nthawi zosayamba ndi zosamaliza; kukhala ndi bwenzi losasintha; yemwe chikondi chake sichisinthayi. Nthawi zonse bwenzi iri limatiganizira ndi kutisamalira. Nanga tidandauliranji ndi kubvutika mumtima? Phunzirani kuchita monga timawerenga ku 1 Petro 5:7, "Kusamala zake zonse; popeza lye amakusamalirani." Mtendere umapezeka nkhondoyo ikatha, bwanji moyo wanu osagonjera kwa Ambuye? Kumbukirani; mukakhulupirira, simudandaula, koma mukadandaula, simukhulupirira. "lnu mudzasunga mtima wokhazikika mu mtendere weni weni, chifukwa ukukhulupirirani inu" Yes. 26:3.

Kusalolera kuli ngati mankhwala okupha (poizoni), amenenso amatichotsera mtendere wa mumtima mwathu. Kumene kumabweretsanzo kukhumudwa ndi chiyembekezo chopanda pake. Nkobvuta kukhululukira amene sanatichitire chilungamo, koma tiyenera kuwakhululukira ngati ifenso tifuna kukhululukidwa. "Koma ngati simukhululukira anthu zolakwa zao, Atate wanunso sadzakukhululukirani zolakwa zanu." Mat. 6:15. Muchotse zoumitsa mtima zonse ndi zobvunduka moyo wanu, ndi kubwezeretsa chikondi ndi chifundo m'malo mwake, ngati inuyo mufuna kulandira chikhululukiro ndi mtendere wopambana wamumtima.

Mwina mukulemedwa ndi zochimwa zanu zakale kuti zachuluka ndipo simungathe kuzisenza. Ngati nkhawa yanu iri imeneyi, mukungoona kudandaula chabe. "Ngati tibvomereza machimo athu, ali wokhulupirika ndi wolungama lye, kuti atikhululukire machismo athu, ndi kutisambitsa kutichotsera chosalungama chiri chonse." 1 Yoh. 1:9 Chotsatira chake, mukhala mu mtendere ndi Mulungu kupyolera mwa Yesu Khristu. "Popeza tsono tayesedwa olungama ndi chikhulupiriro, tikhala  ndi mtendere ndi Mulungu mwa Ambuye wathu Yesu Khristu" Aroma 5:1. Mfumu Davide adachimwa: nayesa kudzilimbitsa mμ msautso wa kuchimwa kwakeko, koma analapa tchimo lake napeza chikhululukiro. Adalola Sing'anga wamkuluyo kumuchiza kupyolera mkubvomereza tchimo, kulapa ndi kukhululukidwa. Mu Salimo 23 akuonetsera chikhulupiriro chake mwa Mulungu ndipo akulongosola momveka uthenga wa mtendere umene iye anaupeza komanso za mtendere ndi chiyanjano chimene chiripo kwa onse amene akhala ndi chiyanjano cheni cheni ndi M'busayo.

I. "Yehova ndiye M'busa wanga: sindidzasowa." M'busa wabwinoyu adapatsa Davide mtendere umene unamkhutiritsa. Koteronso ngati ife tiyamba tafuna ufuinu wa Mulungu," izi zonse zidzaonjezedwa, zosowa zathu zidzakwaniritsidwa.

2. Atipanga ife kukhala ndi mtendere m'dziko lobvutikali. Atitsogolera ife kumalo a phee mchikondi chake chosasintha.

3. Apa Davide akukumbukira nthawi imene adakhala obvutika m'moyo mwake chifukwa cha tchimo. M'busa wabwino adamkhululukira nabwezeretsanso chimwemwe ndi mtendere kwa iye.

4. Ngakhale anamondwe ndi zobvuta za moyo uno zitichulukire, sitidzaopa choipacho chifukwa Mulungu ali nafe kutipulumutsa, kutiteteza ndi kutisamalira.

5. M'busa okoma otani uyu okhoza kutidzaza ife ndi zokoma zosefukura pamaso pa adani athu!

6. Chitetezo choposa chotani chimene nkhosa za pabusa zake ziri nacho! Kodi mumdziwa M'busa ameneyu? Kodi mumkhulupirira lye? Yesaya atiuza kuti M'busa woleza ndi wachifundoyu "Adzasonkhanitsa ana a nkhosa ndi dzanja lake, ndikuwanyamula pa chifuwa chake." Kodi ndinu okonzeka kutulitsidwa mchisokonezo kupita m'manja a mtendere wosatha wa Mulungu? Ndinu okonzeka kodi kutula zochimwa zanu zonse zakale kwa lye, mayesero anu, mantha a tsogolo lanu, ndi kudzipereka kwathunthu kwa lye? Kusankha ndi kwa inu, ndipo ndinu nokha eni amene muyenera kusankha, osati wina ai.

Mukadza kwa Yesu ndi mtima wanu wonse, ndiye kuti mwatsiriza ntchito yonse yofuna-funa mtendere. Adzakupatsani mtendere ndi bata zomwe zichokera kwa lye yekha chifukwa chomukhulupirira.

Apo mudzakhoza kunena monga olemba wina adalemba:

Ndikuudziwa mtendere umene mwa iwo mulibemtendere,
Bata, momwe mphepo za nkuntho zimaomba
Malo obisika komwe maso ndi maso
Ndi Mbuyeyo udidzapita
.

Ralph Spalding Cushman

Mudzakhala ndi mtendere wa mumtima m'dziko la mabvuto! Tsegulani khomo la mtima wanu kwa Yesu - tsopano lino - ndipo tsiku Jina adzakutsegulirani khomo la mmwamba, komwe mtendere weni weni udzakhala nthawi zonse.

Lumikizanani nafe.

Pezani mauthenga olembedwa.

Kodi Ndinu Okhulupirika Bwanji?

Onani, Inu mukondwera ndi zoonadi  m'malo a m'katimo; ( Masalmo 51:6)

Kukhulupirika kumasonyeza kukhala pa choonadi mogwirizana ndi zochita-chita zonse za pa moyo. Kukhulupirika kumachokera mu mtima ndipo ndi chilamulo chokhazikika m'uthenga wa Yesu Kristu. Mulungu amadziwa maganizo ndi zolingirira za mu mtima. Amayang`anira kukhulupirika ngati chilamulo chofunika chifukwa Iye ndi Mulungu wokhulupirika (Deuteronomo 32:4). Iye adzadalitsa kukhulupirika kwathunthu kwa mu mtima wathu.

 

Kodi mumalankhula choonadi pamene mwapezeka kusiyana ndi pamene wina sanadziwe?

Kodi mumaonetsa khalidwe lonyenga m'malo mowonetsa moyo wanu weni-weni?

Kodi mumagula zinthu pa ngongole pamene mukudziwa kuti simungathe kulipira?  

Nkhani yonse ya: Kodi Ndinu Okhulupirika Bwanji?

Kodi mumachita mokhulupirika zonse zomwe mukudziwa kuti Mulungu akufuna kuti mumchitire?

Kodi muli okhulupirika molingana ndi chiphunzitso cha Buku Lopatulika?

Kodi inu ndi munthu amene mumadzi-onetsa kukhala ngati wokhulupirika?

Pali nkhani ina yogwira mtima imene ikupezeka m'chipangano chatsopano ya munthu dzina lake Hanania ndi mkazi wake Safira (Machitidwe 5:1-11). Anagulitsa munda wawo monga anachitira ena, nadzionetsa ngati anapereka ndalama zonse kumpingo, pamene iwo anagwirizana mwanseri kusunga zina. Hanania ndi Safira anabweretsa ndalama kwa akulu a mpingo, iwo ananena kuti anagulitsa pa mtengo womwe anapereka. Kusakhulupirika kwawo kunaweruzidwa nthawi yomweyo ndi chilango cha imfa. Pa nkhaniyi ya mpingo woyambirira, chipha-maso (kusakhulupirika) kunaperekedwa chilango cholimba. Mulungu amayang`ana mosalekerera pa zonama zotero. Ifenso monga Hanania ndi Safira tingachite chinyengo ngakhale sitinalankhule bodza. Timayiwala kuti tidzawerengedwa mlandu pa maso pa Mulungu. Mulungu amadziwa mitima yathu ndipo amayembekeza kukhulupirika kwathunthu.

Munthu wa chiphamaso amadzionetsera ngati wabwino pamene sali choncho. Iye amanena kuti ali pa choonadi, pamene amachita zokhotetsa choonadi kuti asapeze mavuto. Iye amalankhula zosowa za anthu ovutika, koma mavuto adzidzidzi akapezeka sapereka nthawi kapena ndalama. Wina amawoneka ngati akukhudzidwa kweni-kweni ndi achibale ake, pamene akuwanena miseche. Wina amawoneka ngati munthu wokhulupirika, koma akhoza kutenga ndalama za munthu wina akapeza mpata. Iye amakhala akuyesetsa kudzilungamitsa mwa iye yekha kuti ali ndi moyo wa pamwamba pa makhalidwe koposa ena, pamene akuchita mwa chinyengo. Munthu amene angakhale ndi makhalidwe amenewa ndi  wachipha-maso ndi wosakhulupirika.

Nthawi zonse chiphamaso cha munthu chimamvetsa chisoni Mulungu. Yesu anati, “ Anthu awa andilemekeza Ine ndi milomo yao; Koma mtima wao uli kutari ndi Ine” (Mateyu 15:8). Milomo ndi mtima wa munthu ndi kovuta zivomerezana. Kukhulupirika kuchokera m'kati mwa mtima ndi mafungulo opezera chisomo ndi kukomera mtima kwa Ambuye.

Mkristu wowona ndi chitsanzo cha kukhulupirika. Iye amapindula pa za uzimu molingana ndi kukhulupirika kwake pa maso pa Mulungu. Kufunika kwa kukhulupirika pamene tikudziwonetsera kwa  anzathu kuyenera kuchitika mo-samalitsa. M'mawu ndi ntchito zomwe timagwira tiyenera kulolera kudzipereka kwanthuthu kuti tikhale pa choonadi.

Pali phunziro limene tingathe kuphunzira kuchokera pa umboni pamene mphunzitsi anafunsa mnyamata wina, “Kodi ungathe kunena bodza chifukwa cha 5 Kwacha?”

“Ayi mayi,” anayankha mnyamata wamng`ono.

“Kodi ungathe kunena bodza chifukwa cha 15 Kwacha?”

“Ayi mayi,” anayankha mnyamata.

“Kodi ungathe kunena bodza chifukwa cha 150 Kwacha?”

“Ayi mayi,” ndilo linali yankho.

“Kodi ungathe kunena bodza chifukwa cha 150,000 Kwacha?.

“Inde,” ananena yekha mumtima, “Kodi ndingachite nayo chiyani 150,000 Kwacha?”

Pamene  uyu  anali  kusinkha-sinkha,  mnyamata wina wamng`ono amene anali kumbuyo kwake ananena, “Ayi mayi”.

“Ayi, chifukwa chiyani?” anafunsa mphunzitsiyo.

“Chifukwa bodza limakhalabe. Pamene 150,000 Kwacha zonse zatha, ndipo zinthu zomwe zinagulidwa zatha, BODZA limakhalabe chikhalire.

Choonadi ndi chofunika mokwanira kotero kuti ife tiyenera kulola kuwona zovuta chifukwa cha choonadi. Tikataya ungwiro wathu kuti tipewe kuchititsidwa manyazi nthawi ino, ndiye kuti tataya chinthu chopambana. Ndalama zopezeka mwa chinyengo ndi malipiro achabe, chifukwa cha chikumbumtima chodetse-dwa ndi chiweruzo chosatha chimene Mulungu amayika pa tchimo limeneli.

Kodi munganene kuti mukuyenda mu kuwunika kwa Mulungu pamene nthawi yomweyo mukuchita ntchito zoipa monga izi:

- Kusakhululukira abale kapena alongo?

- Kusakonzetsa zolakwika pamene munalakwira ena?

- Kuonjezera nkhani?

- Kuphwanya lonjezo?

- Kuba zake za Mulungu,chachikhumi ndi chopereka?

Kukhulupirika ndi yeso la chikhalidwe. Mulungu amadziwa mitima yathu, ndipo palibe chobisika ndi Iye. Komabe, nthawi zina sitikudziwonetsa kwa Mulungu monga m'mene amatidziwira ndi m'mene tikumvera m'kati mwa mitima yathu. Mwinanso sitimadziwonetsa kwa anthu ena m'mene ife tili. Munthu wa chisangalalo choona ndi iye amene amakhala wokhulupirika kwa Mulungu, ndipo amavomereza m'mene alili. Pamene tikutsegula mitima ndi miyoyo yathu kwa Mulungu mavuto awa angathe kutha.

Zolinga ndi chikhalidwe chathu ziyenera kuyesedwa ndi yeso la choonadi. Kuti tipambane yeso limeneli la zochita-chita zathu ndi Mulungu ndiponso anthu, tikusowa kusinthika m'kati mwathu chifukwa za kunja zimawonetsa za m'kati mwa munthu. Kodi inu ndi munthu wokhulupirika? Mulungu amafunitsitsa choonadi, dzikonso limachiyembekeza, ife tonse timapindula nacho. Ndi moyo wokhawo umene umapindula. “Pofuna kukhala nao makhalidwe abwino” (Ahebri 13:18). “Musabwezere munthu ali yense choipa chosinthana ndi choipa. Ganiziranitu zinthu za ulemu pa maso pa anthu onse” (Aroma 12:17). Wereganinso Levitiko 19:35-36, (“Musamachita chisalungamo poweruza mlandu, poyesa utali wache, kulemera kwache, kapena kuchuruka kwache. Mukhala nacho choyesera choona, miyeso yoona, efa woona, hini woona; Ine ndine Yehova Mulungu wanu…”) ndiponso Miyambo 19:5, (“Mboni yonama sidzakhala yosalangidwa; Wolankhula mabodza sadzapulumuka”).

Lumikizanani nafe.

Pezani mauthenga olembedwa.