Bwanji Za Mankhwala, Zoledzeretsa, Ndi Chiwerewere?

"Pakuti mphotho yake ya uchimo ndi imfa..." (Aroma 6:23)

Tiyeni tinene zoonadi. Zirombo zoopsya kumwa zoledzeretsa, mankhwala ndi chiwerewere ziri  nkuopsyeza ndiponso kuononga chimene Mulungu anachilenga kukhala chokoma ndiponso chabwino. Monga mchitidwe wa Octopus wamphamvuyo, izi zimakoka ang'ono komanso aakulu ndi kuwafumbatira.

Anthu ambiri amakakamizidwa pambali iliyonse ndi zokhumba zao, monga manyuzi pepala komanso ndi kuitanira kwa television. Maso ndi makutu zimalunjika kumene kuli zosokoneza zokhazokha zomwe zotsatira zake ndi kukhala ndi moyo wa uzimu komanso wa kuthupi wobwerera m'mbuyo. Temberero la chakumwa choledzeretsa, mankhwala ndi chiwerewere zaleka chitsanzo chokoma cha m’midzi yathu popanda kuongoledwa ndipo ziri nkupita ku chionongeko.

Kodi nanga ndi mbadwo wokha wa ana womwe utsutsidwe? Ayi. Naonso makolo ambiri asiyanso chikhalidwe chokoma, natsata chikhalidwe choipa, machismo ambiri ochitidwa ndi ana ambiri lero, makolo awo amangowalekerera osadziwa kuti alikupanga ana awo kuti adzakhale zidakwa, ogwiritsa ntchito mankhwala osaloledwa, ndi osuta pakulephera iwo kudzudzula pa kumwa zoledzeletsa ndi kusuta.

Mwadala, pakufuna kukhala osamvera malamulo olunjika a Mulungu makolo naonso ali pa njira yotsetsereka yopita ku mnyozo panopa komanso moyo ulinkudzawo. Kulira kopfuula kuyenera kukwera kumwamba. Tingadzipulumutse bwanji ife ndi ana athu?

M'manyumba mwathu, m'masukulu ndiponso m’makoleji sangathe kutulutsa chitsanzo chabwino choyenera nzika za dziko monga momwe maiko athu afunira ngati kumwa zoledzeretsa ndi kugwiritsa ntchito mankhwala zirigoyang'anidwa ndi kulimbikitsidwa ndi makolo opanda chikhalidwe chabwino, aphunzitsi ndi iwo anzeru zakuya . (Professors}, kuonongeka kwachikhalidwe chabwino m'masukulu kuli nkuopsezanso. Sipanathe zaka zambiri pamene aphunzitsi ndi anzeru zakuya akadachotsedwa ntchito chifukwa cholekerera ana asukulu kukhala ndi makhalidwe oipa.

Mliri umene watenga malo kwambiri mbadwo wathu uno ndi kumwa mwa uchidakwa kumenenso kumaononga chikhalidwe chabwino. Kuononga chikhalidwe ndi kumwaza ndalama pamene miyanda miyanda ya anthu alikusowa chakudya. Ichi ncha umphawi komanso chopereka magawano m'manyumba mwathu, ndiponso lonyoza dalitso loyera la Mulungu pa mtundu wa anthu.

Nkhani yonse ya: Bwanji Za Mankhwala, Zoledzeretsa, Ndi Chiwerewere?

Kuphatikiza kuipa kwa kumwa zoledzeretsa kwaonjezeranso kagwiritsidwe ka mankhwala osaloledwa. Kuipa kwa mankhwalawa kumaposa phindu lomwe mankhalawa amapereka. Kugwiritsa ntchito mankhwala osaloledwawa kungapangitsenso kuweruza molakwika ndiponso kuonongeka kwa nzeru. Ogwiritsa ntchito mankhwalawa naonso amabvomereza kuti ndi ulendo waku imfa mu nzeru, kuthupi lanyama, mu mzimu komanso kungathe kuononga ubongo. Kuphana ndi kudzipha ndizo zotsatira zake zoopsya za mchitidwe umenewu.

Khristu, m"Chipangano Chatsopano, anaika chitsanzo cha makhalidwe abwino. Naikanso ndime ya chikhalidwe chabwino. Mulungu analenga munthu kuti mtundu wa anthu uchuluke ndi kuti anthu adzikwatirana mwamuna ndi mkazi. lye anaikanso kuti padzikhala kufunana koyenera pa moyo Wa m’banja. Ukwati uchitidwe ulemu ndi onse, ndi pogona pakhale posadetsedwa; koma adama ndi achigololo adzawaweruza Mulungu. Aheb. 13:4

Anthu ambiri ali kuzunzika ndi miZimu ya chilakolako. Zotsatira zake zimakhala nkhondo yeniyeni pakati pa thupi ndi Mzimu. Thupi limafuna kukhala ndi ufulu wa kuchita zokondweretsa zake popanda choletsa, pamene Mzimu amadziwa bwino kuti malamulo onse a Mulungu ayenera kutsatidwa bwino. Chiwerewere sichingathe kuthetsa kutentha mtima kwa chilakolako, monganso mowa wa whisky umalephera kuchotsa ludzu la mowa. Apa choonadi ndiye chili pa mbali ina osati iyi ayi.

Chiwerewere, chigololo, dama la amunaokhaokha ndi chiwerewere china chirichonse pakati pa munthu ndi nyama ndi choletsedwa m'Mawu a Mulungu. Chiwerewere chimabweretsa kuwawa, kupweteka mtima, umphawi, kuchimwa, ndiponso kutenga matenda. Lev 18:23, Agalatiya 5.19-21. Chiyero chimabweretsa chisoni kuti anthu oyenera ndi olongosoka ali kukhala mu umphawi pamene munthu wopanda pache ali nazo zonse zomuyenereza. Mtumwi Paulo m'buku la Aroma akunena za momwe Mulungu adzaweruzire ochita chiwerewere cha amuna okhaokha. Chifukwa cha ichi, Mulungu nawapereka iwo ku zilakolako za manyazi: Pakuti ngakhale akazi awo anasandutsa machi- tidwe awo achibadwidwe kukhala osalingana ndi chibadwidwe: Chimodzimodzinso amuna, anasiya chikhalidwe cha chibadwidwe cha akazi, natenthetsana wina ndi mzake, amuna okhaokha ndi kuchita cbosayenera kuti akalandire mphoto yoywera m'chitidwe umenewu. Monga momwe iwo sanafuna kukhala naye Mulungu m'nzeru zao .. Mulungu anawapereka ku mtima wokanika, kuchita zosayenera: Pakudziwa chiweruzo cha Mulungu, kuti ochita zimenezi ayenera kufa, chifukwa samangodzichita kokha ayi, komanso amakondwera nazo. (Aroma 1:26,28,32). Ili linali tchimo lonyansa kwambiri la Sodomu ndi Gomora limene linabweretsa kulanga kwa Mulungu pakati pawo (Gen. 19). Monga mwa Malemba Oyera kuti nkovuta kuti Mzimu Woyera kubwereranso m 'mitima yathu ndi kukhal m'moyo wa Chikristu ngati tiri kukhala natichitabe machimo amenewa.

Mkati mwa chiwerewerechi ndi khungu la uzimu, la tchimo lomwe kuli kusowa manyazi pakusapembedza Mulungu, tiyenera kutembenukira ku Buku Lopatulika lomwe liri ndi udindo wonse wosakaikitsa wa muyaya pa chabwino kapena choipa.

Wokondedwa wowerengawe, kukhala ndi moyo wokondwa, ndi inuyo kukhala ndi mtendere ndi Mulungu, muyenera kudza m'chiyanjano pamodzi ndi lye.

Chigonjetso chiri kukuyembekezani! Muyenera kuzindikira ndi kulapa kuti muli ochimwa ndipo mukhulupilire kuti Yesu anafa pa mtanda atasenza tchimo lanu. Pamene mutsegula mtima wanu kwa Mulungu ndi kulapa machimo anu, lye adzakukhululukarani. Ngati tibvomereza machimo athu, lye ali wokhulupirika ndi wolungama kutikhululukira ife machismo athu, ndi kutisambitsa kutichotsera chosalungama chirichonse.

Muyenera kupereka mtima wanu wonse kwa Yesu, Mpulumutsi wanu, ndipo tsatirani bwino pomvera Mau Ake ndi Mzimu Woyera. Madalitso a moyo wosinthika ndi maganizo oyera omwe amabweretsa kusinthika kotheratu m'zochita zanu. Khristu adzakulimbitsani mtima pokomana ndi mabvuto a moyo ndi mphamvu yogonjetsa mayesero omwe angakuzungu- lireni. ldzani kwa Yesu tsopano pamene mumva kuitana kwake. "Funani Yehova popezekalye, itanani lye pamene ali pafupi. ... "  (Yesaya 55:6).

Lumikizanani nafe.

Pezani mauthenga olembedwa.