Kodi Ndinu Okhulupirika Bwanji?

Onani, Inu mukondwera ndi zoonadi  m'malo a m'katimo; ( Masalmo 51:6)

Kukhulupirika kumasonyeza kukhala pa choonadi mogwirizana ndi zochita-chita zonse za pa moyo. Kukhulupirika kumachokera mu mtima ndipo ndi chilamulo chokhazikika m'uthenga wa Yesu Kristu. Mulungu amadziwa maganizo ndi zolingirira za mu mtima. Amayang`anira kukhulupirika ngati chilamulo chofunika chifukwa Iye ndi Mulungu wokhulupirika (Deuteronomo 32:4). Iye adzadalitsa kukhulupirika kwathunthu kwa mu mtima wathu.

 

Kodi mumalankhula choonadi pamene mwapezeka kusiyana ndi pamene wina sanadziwe?

Kodi mumaonetsa khalidwe lonyenga m'malo mowonetsa moyo wanu weni-weni?

Kodi mumagula zinthu pa ngongole pamene mukudziwa kuti simungathe kulipira?  

Nkhani yonse ya: Kodi Ndinu Okhulupirika Bwanji?

Kodi mumachita mokhulupirika zonse zomwe mukudziwa kuti Mulungu akufuna kuti mumchitire?

Kodi muli okhulupirika molingana ndi chiphunzitso cha Buku Lopatulika?

Kodi inu ndi munthu amene mumadzi-onetsa kukhala ngati wokhulupirika?

Pali nkhani ina yogwira mtima imene ikupezeka m'chipangano chatsopano ya munthu dzina lake Hanania ndi mkazi wake Safira (Machitidwe 5:1-11). Anagulitsa munda wawo monga anachitira ena, nadzionetsa ngati anapereka ndalama zonse kumpingo, pamene iwo anagwirizana mwanseri kusunga zina. Hanania ndi Safira anabweretsa ndalama kwa akulu a mpingo, iwo ananena kuti anagulitsa pa mtengo womwe anapereka. Kusakhulupirika kwawo kunaweruzidwa nthawi yomweyo ndi chilango cha imfa. Pa nkhaniyi ya mpingo woyambirira, chipha-maso (kusakhulupirika) kunaperekedwa chilango cholimba. Mulungu amayang`ana mosalekerera pa zonama zotero. Ifenso monga Hanania ndi Safira tingachite chinyengo ngakhale sitinalankhule bodza. Timayiwala kuti tidzawerengedwa mlandu pa maso pa Mulungu. Mulungu amadziwa mitima yathu ndipo amayembekeza kukhulupirika kwathunthu.

Munthu wa chiphamaso amadzionetsera ngati wabwino pamene sali choncho. Iye amanena kuti ali pa choonadi, pamene amachita zokhotetsa choonadi kuti asapeze mavuto. Iye amalankhula zosowa za anthu ovutika, koma mavuto adzidzidzi akapezeka sapereka nthawi kapena ndalama. Wina amawoneka ngati akukhudzidwa kweni-kweni ndi achibale ake, pamene akuwanena miseche. Wina amawoneka ngati munthu wokhulupirika, koma akhoza kutenga ndalama za munthu wina akapeza mpata. Iye amakhala akuyesetsa kudzilungamitsa mwa iye yekha kuti ali ndi moyo wa pamwamba pa makhalidwe koposa ena, pamene akuchita mwa chinyengo. Munthu amene angakhale ndi makhalidwe amenewa ndi  wachipha-maso ndi wosakhulupirika.

Nthawi zonse chiphamaso cha munthu chimamvetsa chisoni Mulungu. Yesu anati, “ Anthu awa andilemekeza Ine ndi milomo yao; Koma mtima wao uli kutari ndi Ine” (Mateyu 15:8). Milomo ndi mtima wa munthu ndi kovuta zivomerezana. Kukhulupirika kuchokera m'kati mwa mtima ndi mafungulo opezera chisomo ndi kukomera mtima kwa Ambuye.

Mkristu wowona ndi chitsanzo cha kukhulupirika. Iye amapindula pa za uzimu molingana ndi kukhulupirika kwake pa maso pa Mulungu. Kufunika kwa kukhulupirika pamene tikudziwonetsera kwa  anzathu kuyenera kuchitika mo-samalitsa. M'mawu ndi ntchito zomwe timagwira tiyenera kulolera kudzipereka kwanthuthu kuti tikhale pa choonadi.

Pali phunziro limene tingathe kuphunzira kuchokera pa umboni pamene mphunzitsi anafunsa mnyamata wina, “Kodi ungathe kunena bodza chifukwa cha 5 Kwacha?”

“Ayi mayi,” anayankha mnyamata wamng`ono.

“Kodi ungathe kunena bodza chifukwa cha 15 Kwacha?”

“Ayi mayi,” anayankha mnyamata.

“Kodi ungathe kunena bodza chifukwa cha 150 Kwacha?”

“Ayi mayi,” ndilo linali yankho.

“Kodi ungathe kunena bodza chifukwa cha 150,000 Kwacha?.

“Inde,” ananena yekha mumtima, “Kodi ndingachite nayo chiyani 150,000 Kwacha?”

Pamene  uyu  anali  kusinkha-sinkha,  mnyamata wina wamng`ono amene anali kumbuyo kwake ananena, “Ayi mayi”.

“Ayi, chifukwa chiyani?” anafunsa mphunzitsiyo.

“Chifukwa bodza limakhalabe. Pamene 150,000 Kwacha zonse zatha, ndipo zinthu zomwe zinagulidwa zatha, BODZA limakhalabe chikhalire.

Choonadi ndi chofunika mokwanira kotero kuti ife tiyenera kulola kuwona zovuta chifukwa cha choonadi. Tikataya ungwiro wathu kuti tipewe kuchititsidwa manyazi nthawi ino, ndiye kuti tataya chinthu chopambana. Ndalama zopezeka mwa chinyengo ndi malipiro achabe, chifukwa cha chikumbumtima chodetse-dwa ndi chiweruzo chosatha chimene Mulungu amayika pa tchimo limeneli.

Kodi munganene kuti mukuyenda mu kuwunika kwa Mulungu pamene nthawi yomweyo mukuchita ntchito zoipa monga izi:

- Kusakhululukira abale kapena alongo?

- Kusakonzetsa zolakwika pamene munalakwira ena?

- Kuonjezera nkhani?

- Kuphwanya lonjezo?

- Kuba zake za Mulungu,chachikhumi ndi chopereka?

Kukhulupirika ndi yeso la chikhalidwe. Mulungu amadziwa mitima yathu, ndipo palibe chobisika ndi Iye. Komabe, nthawi zina sitikudziwonetsa kwa Mulungu monga m'mene amatidziwira ndi m'mene tikumvera m'kati mwa mitima yathu. Mwinanso sitimadziwonetsa kwa anthu ena m'mene ife tili. Munthu wa chisangalalo choona ndi iye amene amakhala wokhulupirika kwa Mulungu, ndipo amavomereza m'mene alili. Pamene tikutsegula mitima ndi miyoyo yathu kwa Mulungu mavuto awa angathe kutha.

Zolinga ndi chikhalidwe chathu ziyenera kuyesedwa ndi yeso la choonadi. Kuti tipambane yeso limeneli la zochita-chita zathu ndi Mulungu ndiponso anthu, tikusowa kusinthika m'kati mwathu chifukwa za kunja zimawonetsa za m'kati mwa munthu. Kodi inu ndi munthu wokhulupirika? Mulungu amafunitsitsa choonadi, dzikonso limachiyembekeza, ife tonse timapindula nacho. Ndi moyo wokhawo umene umapindula. “Pofuna kukhala nao makhalidwe abwino” (Ahebri 13:18). “Musabwezere munthu ali yense choipa chosinthana ndi choipa. Ganiziranitu zinthu za ulemu pa maso pa anthu onse” (Aroma 12:17). Wereganinso Levitiko 19:35-36, (“Musamachita chisalungamo poweruza mlandu, poyesa utali wache, kulemera kwache, kapena kuchuruka kwache. Mukhala nacho choyesera choona, miyeso yoona, efa woona, hini woona; Ine ndine Yehova Mulungu wanu…”) ndiponso Miyambo 19:5, (“Mboni yonama sidzakhala yosalangidwa; Wolankhula mabodza sadzapulumuka”).

Lumikizanani nafe.

Pezani mauthenga olembedwa.